M’MENE MABOMA ANGAKONZEKELERE EL NIÑO WAMPHAMVU
Zotsatira za El Niño wamphamvu zimasiyana kwambiri malinga ndi madera. Madera a Chigawo cha Kumpoto nthawi zambiri amakhala ndi chiopsezo chochepa, ndipo chiopsezo cha ng’amba ndi mvula yambiri chimakhala chochepa komanso chiopsezo cha chilala chimakhala chochepa mpaka chapakatikati.
Madera a Chigawo cha Pakati ali ndi chiopsezo chosiyanasiyana cha nyengo ya ng’amba komanso chilala chapakatikati, pomwe chiopsezo cha mvula yambiri chimakwera m'maboma ngati Ntchisi ndi Dowa.
Chigawo cha Kumwera chili ndi chiopsezo chachikulu komanso chophatikizana: maboma khumi ndi awiri amakumana ndi nyengo ya ng’amba yapakatikati, Chilala champhamvu, komanso chiopsezo cha mvula yambiri nthawi imodzi, zomwe zikutanthauza kuti njira zothanirana ndi chilala komanso kusefukira kwa madzi ziyenera kukonzedwa zonse.