CAP Alert · Actual

NAMONDWE JUDE KUM'MWERA NDI PAKATI

Expired: Tropical storm
Extreme severity
Urgency Expected
Severity Extreme
Certainty Likely
Category Met
Language en
Time period
  • Issued 08 Mar 2025 22:57
  • Effective 08 Mar 2025 22:57
  • Onset 10 Mar 2025 07:00
  • Expires 14 Mar 2025 23:00
Severity
Extreme
Severe
Moderate
Minor

NAMONDWE JUDE KUM'MWERA NDI PAKATI

Area

Zigawo za kum'mwera ndi pakati

Event description

Nthambi Yoona Zanyengo ndi Kusintha kwa Nyengo ikudziwitsa mtundu wa a Malawi kuti dera lopepuka lomwe lili munyanja ya India tsopano lakula mphamvu ndipo likutchedwa Namondwe JUDE. JUDE akuyembekezeka kufika ku Mozambique lamulungu chakumadzulo kudutsira pakati pa Beira ndi Nampula. Namondweyu akuyembekezereka kukhudza kwambiri m’madera am’chigawo chakum’mwera kwa Malawi ndi mvula yoposera mlingo wa 100mm m’maola 24 kuyambira lolemba pa 10 March 2025. M’madera omwe angakhudzidwe kwambiri ndi awa : Mulanje, Phalombe, Chiradzulu, Thyolo, Zomba, Blantyre, Balaka, Ntcheu, Machinga, Neno, Mwanza, Nsanje ndi Chikwawa . Ziopsezo: 1. Mvula ya mphamvu ndi ya mvumbi 2. Madzi osefukira mwadzidzidzi 3. Mphepo ya mkuntho 4. Kuonongeka kwa katundu 5. Kuvulala kwa anthu ngakhalenso kumwalira

Instructions

Malangizo: • Ngati madzi angasefukire mdera lanu samukirani m’madera okwera. • Pofunika kukhala motalikirana ndi mitsinje pomwe kukugwa mvula ya mphamvu chifukwa madzi akhoza kusefukira modzidzimutsa. • Ngati nkotheka pewani kuyendetsa galimoto pomwe kuli mphepo yamphamvu kwambiri. Nthambi Yoona Zanyengo ndi Kusintha kwa Nyengo ipitiriza kulondola kayendedwe ka Namondwe JUDE ndi kudziwitsa mtundu wa a Malawi.