CAP Alert · Actual
Mvula ya mphamvu kum'mwera
Mvula ya mphamvu kum'mwera kwa Malawi
Chigawo cha kumwera
Madera ambiri am'chigawo cha kum'mwera akuyembekezeka kulandira mvula yochuluka yoposa mlingo wa 50 mm pa tsiku (ma ola 24) zomwe zikupereka ziopsezo za: 1. kusefukira kwa madzi mwadzidzidzi. 2. Kugwa kwa nyumba komanso zimbuzi.
● Madzi osefukira mwadzidzidzi: Tikhale tcheru ndipo tipewe kuoloka madzi osefukira kapena othamanga kuti titeteze miyoyo yathu. ● Mvula ya Mabingu: Kukamagwa mvula ya mabingu tikuyenera kubisala pamalo otetezeka bwino ndipo tipewe kubisala pansi pa mitengo. ● Chinyezi: Tikhale osamala ndi nyumba kapena zimbuzi zomwe zanyowa kwambiri ndi mvula chifukwa zitha kugwa nthawi ina iliyonse.