KUCHOTSA CHENJEZO LA NAMONDWE JUDE
March 8, 2025, 10:57 p.m.
NAMONDWE JUDE KUM'MWERA NDI PAKATIKUCHOTSA CHENJEZO LA NAMONDWE JUDE
-
Issued Fri 14 Mar 2025 11:10
-
Effective: Fri 14 Mar 2025 11:10
-
Expires: Fri 14 Mar 2025 12:00
KUCHOTSA CHENJEZO LA NAMONDWE JUDE! Tsiku ndi nthawi yosindikizira: Lachinayi pa 13 March, 2025; 10 koloko m’mawa. Kusindikiza kwa nambala 31 (No.2024/25-31). Nthambi Yoona za Nyengo ndi Kusintha kwa Nyengo ikudziwitsa mtundu wa Malawi kuti Namondwe JUDE tsopano ali kutali ndi dziko la Malawi ndipo pakadali pano sakuperekanso chiopsezo ku dziko lino. Nthambi Yoona za Nyengo ndi Kusintha kwa Nyengo ipitiriza kulondoloza Namondweyu ndi kukudziwitsani pakakhala kusintha kulikonse. Padakali pano, madera ambiri a mdziko muno, makamaka madera okwera a mchigawo cha kumpoto, madera a m’mphepete mwa nyanja ya Malawi ndi enanso a amchigawo cha pakati, akuyembekezeka kulandira mvula yochuluka m’masiku angapo akudzawa kamba ka dera la mkumano wa mphepo lotchedwa ITCZ. Chiopsyezo cha kusefukira kwa madzi mwadzidzidzi chikuyembekezeka kukhala chokwera m’madera am’chigawo cha kumpoto, choncho, tikhale tcheru.