NYENGO MSABATAYI Yatulutsidwa : 08 November 2026 | Kuyambira pa 9 mpaka 15 November, 2026

Weekly Weather Update

NYENGO M’SABATA IKUBWERAYI

M’sabatayi, tiyembekezere mvula m’madera ochulukirapo m’chigawo cha kumpoto ndi m’chigawo cha pakati kuyelekeza ndi m’chigawo chakum’mwera (Chithunzi 1). Nyengo yotentha kwambiri ipitilira m’madera ambiri.

Lolemba mpaka Lachitatu, kudzakhala mitambo yapatalipatali, mvula ya mabingu m’madera ochepa, ndi mphepo ya mphamvu m’madera ena. Izi zikhala chonchi kamba ka mkumano wa mphepo zochokera kumpoto cha kumvuma komanso zina zochokera kumwera cha kumvuma.

Kuyambira Lachinayi, dera la mpweya opepuka (lomwe likuyembekezeka kubuka ku Mozambique Channel) lidzalimbikitsa mvula ya mabingu m’madera ambiri makamaka m’chigawo cha kumpoto, madera a m’bali mwa nyanja ya Malawi, ndi madera ena a m’chigawo chapakati. Mvula ya mabinguyi ingadzathe kugwanso m’madera ochepa a m’chigawo cha kumwera.

Mwera wa mphamvu akuyembekezeka pa nyanja choncho asodzi ndi ena onse ogwiritsa ntchito nyanja akhale osamala.