NYENGO M’SABATA IKUBWERAYI
Kuyambira lolemba mpaka lachitatu pa 1 April 2026, tiyembekezere nyengo ya mvula ya mabingu m’madera ochepa yomwe idzigwa ya mphamvu maka m'madera a m’phepete mwa nyanja ya Malawi kamba ka mphepo zosakhazikika zochokera kumvuma. Koma Pofika lachinayi Mphepozi zidzakhala zikukumana ndi zina zochokera kumwera chakumvuma ndipo izi zidzapangitsa madera ambiri kukhala ndi nyengo ya mphepo, yozizira komanso mvula yomwe ikuyembekezereka kugwa yamphamvu m’madera ambali mwa Nyanja ya Malawi monga Nkhotakota, NkhataBay, Karonga.