Nyengo msabata ikubwerayi 29 Dec 2025 - 4 Jan 2026

Weekly Weather Update

NYENGO M’SABATA IKUBWERAYI

Tiyembekezere nyengo ya mvula kupitirira ndipo yamphamvu ikuyembekezeka mphepete mwa nyanja ya Malawi ndi madera ena amchigawo chakumpoto ndi pakati. Izi zikhala chonchi kamba ka dela lodzetsa mvula lotchedwa ITCZ lomwe likhale lili mdziko muno. Mvula ikuyembekezeka kupitirira mlingo wa 120mm ku Nkhotakota ndi Nkhatabay, umene uli mlingo opitirira mmene mvula imagwera mmaderawa munthawi ino. Izi zikubweretsa chiopsezo cha madzi osefukila.

Mphepo ya Mwera ikhala ikuomba nthawi zina pa nyanja zathu mu sabatayi.