
MALANGIZO M’SABATALI
●Madzi osefukira mwadzidzidzi (flash floods):Tikhale tcheru ndipo tipewe kuoloka madzi osefukira kapena othamanga kuti titeteze miyoyo yathu
●Mvula ya Mabingu: Kukamagwa mvula ya mabingu tikuyenera kubisala pamalo otetezeka bwino ndipo tipewe kubisala pansi pa mitengo.
●Chinyezi: Tikhale osamala ndi nyumba kapena zimbuzi zomwe zanyowa kwambiri ndi mvula chifukwa zitha kugwa nthawi ina iliyonse.
●Kutelera kwa mseu ndi khungu: Tipewe kuyendetsa galimoto mothamanga kwambiri pamseu ndi kupitiliza kutsatira mwachidwi mauthenga onse a zanyengo pamene mvula ikupitilira kugwa.