
⛈💨🌊☂️Tiyembekezere nyengo ya mitambo yapatalipatali komanso yozizilirako m’madera ambiri komanso mvula yomwe igwe yamphamvu maka m’madera akumpoto m’mphepete mwa nyanja ya Malawi kamba ka mphepo zachinyotho ndi zosakhazikika zochokera kumvuma.
Koma kuyambira Lachisanu pa 02 May 2025, mvula ya mphamvu ikuyembekezereka kufalikira m’madera ambiri komanso mphepo ya mwera yomwe izidzaomba pa Nyanja ya Malawi ndi nyanja zina kamba ka mphepo zochokera kum’mwera cha kumvuma.