NYENGO M’SABATA IKUBWERAYI 20-26 July 2026
Kuyambira Lolemba mpaka Lachisanu, tiyembekezere nyengo yopanda mitambo komanso yozizira usiku ndi m’mawa madera ambiri. Kudzikhala nyengo yofunda komanso yadzuwa nthawi ya masana. Izi zikhala chonchi kamba kadera la mpweya olemera omwe wakhazikika pamtunda omwe ukukanikitsa kapangidwe ka mitambo.
Kuyambira Loweruka mpaka Lamulungu kudzakhala nyengo ya mphepo komanso yamitambo ndi mvula yamawawa komanso yowaza m’madera ochepa kamba ka mphepo za chinyontho chochuluka kuchokera ku m’mwera chakumvuma m'nyanja ya mchere ya India.