Nyengo msabata ikubwerayi 20 - 26 Jan 2025

Weekly Weather Update

Sabatayi ikuyembekezeka kukhala ya mvula m’madera ochuluka kamba ka dera lodzetsa mvula la ITCZ mothandizana ndi mphepo za chinyontho zochokera ku Congo.

Palinso, kuthekera kwakukulu kwa dera la mpweya opepuka kubadwa m’nyanja ya m’chere ya India ya pakati pa mayiko a Mozambique ndi Madagascar (yomwe imatchedwanso kuti Mozambique Channel) pafupi ndi doko la Beira cha kumathero a’sabatayi zomwe zikuyembekezeka kudzalimbikitsa nyengo ya mvula m’madera ambiri makamaka am’zigawo za pakati ndi kum’mwera.

Zimenezi zikupereka chiopsezo cha madzi osefukira mwadzidzidzi m’madera otsika ndi malo ena omwe amasefukira madzi kawirikawiri.