NYENGO M’SABATA IKUBWERAYI
Tiyembekezere nyengo yamvula ya mabingu m’madera ambiri yomwe idzigwa ya mphamvu maka m'madera am’phepete mwa nyanja ya Malawi monga ku Salima ndi madera ozungulira kuyambira pa 16 March mpaka lachitatu pa 18 March 2026 kamba ka dera la mphweya lopepuka lomwe lili m’dziko muno. Kenako, mvula idzayamba kuchepa mphamvu mpaka kumapeto a sabatayi.