NYENGO M’SABATA IKUBWERAYI
Tiyembekezere nyengo yozizirapo, yamphepo komanso yamitambo ndi mvula ya mabingu yomwe idzigwa ya mphamvu maka m'madera am’phepete mwa nyanja ya Malawi msabatayi kamba ka dera logwetsa mvula lotchedwa ITCZ lomwe likuyembekezereka kukhazikika m’dziko muno.
Mphepo ya mwera ikuyembekezereka kuomba mwamphanvu pa nyanja ya Malawi ndi nyanja zina.