Nyengo msabata ikubwerayi 06-12 April 2026

Weekly Weather Update

NYENGO M’SABATA IKUBWERAYI

Tiyembekezere nyengo ya mitambo ya patalipatali ndi mvula yamphamvu yamabingu ipitirira m’madera ochepa makamaka a mphepete mwanyanja ya Malawi, monga ku Karonga kuyambira Lolemba pa 6 April mpaka Lachitatu pa 8 April 2026.

Lachinayi pa 9 April 2026, tiyembekezere nyengo yamphepo, yozizira komanso mvula yomwe ikhonza kufalikira m’madera ena achigawo chakumwera komanso pakati koma yamphamvu m’madera ochepa a mphepete mwanjanja.