NYENGO M’SABATA IKUBWERAYI
Tiyembekezere nyengo ya mitambo komanso ya mvula ya mabingu yomwe izigwa momvelera m’madera ambiri amdziko muno, koma mvula yochulukirapo mlingo ikuyembekezeka kuyambira la lachisanu pa 06 March 2026. Izi zikhala chonchi kamba ka mphepo zomwe zizifika mdziko muno kuchokera m’nyanja ya mchere ya India chakumvuma.