“Tayambapo kauniuni wa kagwedwe ka mvula ka Dzinja likubwerari” -Nthambi ya Zanyengo.

12 Aug, 2024 News

WhatsApp Image 2024-08-12 at 11.43.48

Nthambi Yowona Zanyengo ndi Kusintha kwa Nyengo mdziko muno, lero, pa 12 August, 2024 yayamba kauniuni wakagwedwe ka mvula m’nyengo ya Dzinja likubwerari la 2024/2025 ndi thandizo lochokera ku Malawi Red Cross Society ndi Trócaire Malawi. Malingana ndi m’modzi wa akuluakulu ku nthambiyi, a Keenness Mang’anda, ntchito yolosera nyengo ya dzinjali ayigwira mwakhama ndi mwaukadaulo monga mwa nthawi zonse ndipo ikuyembekezeka kutha pofika sabata ya chiwiri ya mwezi wa September.

Chaka chatha, nthambiyi inalosera kuti mvula imayembekezeka kugwa mwanjomba komanso madera ambiri amayembekezera ng’amba yoopsa mu Dzinja lathari kamba ka ElNino zomwe zinachitikadi. Koma a Keenness Mang’anda ati ulendo uno pali kuthekera kwakukulu kwakuti madera ena makamaka am’zigawo zapakati ndi kum’mwera alandira mvula yoposa mulingo okhazikika kamba ka LaNina. Komabe, tsatanetsatane wa kagwedwe ka mvula afotokozedwa mu ulosi omwe ukuphikidwawu. Zinthu zomwe zikuyembekezeka kuloseredwa mu Ulosiwu ndi monga: masiku olandirira mvula yodzalira, mulingo wa mvula, kutalika kwa nyengo ya Dzinja mongotchulapo zochepa.

20240812_110357

Yobu Kachiwanda yemwenso ndi m’modzi wa akuluakulu ku Nthambi Yowona Zanyengoyi ati Ulosi wa mvulawu udzafalitsidwa m’mwezi wa September akangomaliza kuwuthyakula ndi cholinga chokonzekeretsa a Malawi munthawi yake.

Chaka ndi chaka nyengo ya dzinja isanafike, Nthambi Yowona Zanyengo ndi Kusintha kwa Nyengo imagwira ntchito yotamandika yolosera kagwedwe ka mvula ndi cholinga chopulumutsa miyoyo ya a Malawi komanso kupititsa patsogolo chuma cha dziko. Ulosi wa dzinjawu umagwiritsidwa ntchito mosiyanasiyana monga pokonzekera ulimi, ku nkhani zokhuza magetsi, ngozi zogwa mwadzidzidzi ndi za umoyo.