NAMONDWE JUDE KUM'MWERA NDI PAKATI
NAMONDWE JUDE KUM'MWERA NDI PAKATI
-
Issued Sat 08 Mar 2025 22:57
-
Effective: Sat 08 Mar 2025 22:57
-
Onset: Mon 10 Mar 2025 07:00
-
Expires: Fri 14 Mar 2025 23:00
Zigawo za kum'mwera ndi pakati
Nthambi Yoona Zanyengo ndi Kusintha kwa Nyengo ikudziwitsa mtundu wa a Malawi kuti dera lopepuka lomwe lili munyanja ya India tsopano lakula mphamvu ndipo likutchedwa Namondwe JUDE. JUDE akuyembekezeka kufika ku Mozambique lamulungu chakumadzulo kudutsira pakati pa Beira ndi Nampula. Namondweyu akuyembekezereka kukhudza kwambiri m’madera am’chigawo chakum’mwera kwa Malawi ndi mvula yoposera mlingo wa 100mm m’maola 24 kuyambira lolemba pa 10 March 2025. M’madera omwe angakhudzidwe kwambiri ndi awa : Mulanje, Phalombe, Chiradzulu, Thyolo, Zomba, Blantyre, Balaka, Ntcheu, Machinga, Neno, Mwanza, Nsanje ndi Chikwawa . Ziopsezo: 1. Mvula ya mphamvu ndi ya mvumbi 2. Madzi osefukira mwadzidzidzi 3. Mphepo ya mkuntho 4. Kuonongeka kwa katundu 5. Kuvulala kwa anthu ngakhalenso kumwalira