Ulosi Wa Nyengo Ya Dzinja Wa Chaka Cha 2025/2026

Sept. 15, 2025
131

Mau oyamba

Nyengo ya dzinja ku Malawi kuno imayamba mu October kufikira m’mwezi wa April. Nthambi yoona za nyengo ndi kusintha kwa nyengo ndiyomwe ili ndi ntchito yopanga kalondolondo/kauniuni wa zinthu zomwe zimabweretsa mvula m’dziko muno. Nyengo ya dzinja imakhazikika m’mwezi wa November kuyambira kumwera kwadziko lino ndipo pang’ono ndi pang’ono imafalikira m’zigawo zapakati komanso kumpoto. Mvula ya Chizimalupsya ndiyomwe imayambilira kugwa nyengo yadzinja isanakhazikike.

Zomwe zimabweretsa mvula ku Malawi

Zinthu zikuluzikulu zomwe zimabweretsa mvula ndi monga nkumano wa mphepo zakum’mwera ndi zakumpoto kwa Africa, mpweya ochokera m’dera la Congo, m’pweya osakhazikika ochokera kumvuma, nkumano wa mphepo zozizira ndi zofunda kuchokera m’dera limodzi monga kum’mwera kokhakokha kapena kum’poto kwa Africa, kulemela ka m’pweya, mphepo za m’mwamba osaiwalanso katenthedwe ka madzi a m’nyanja zikuluzikulu monga za Pacific, India komanso Atlantic.

ULOSI WA EL NINO KAPENA LA NINA

Njira zolosera nyengo padziko lonse zikuonetsa kuti gawo lalikulu la dzinja la 2025/2026 silikhudzidwa kwambiri ndi katenthedwe (El Niño) kapena kazizilidwe (La Niña) ka madzi cha kum’mawa kwa nyanja ya mchere ya Pacific, kutanthauza kuti mlingo wake ndi wa pakatikati. Komabe pali kuthekera koti miyezi ina yochepa idzakhudzidwa ndi La Niña. Zaka zodziwika zimene mbiri yake ikhoza kuyerekezedwa ndi dzinja la 2025/2026 ndizo; 1996/1997, 2013/2014, 2016/2017 ndi 2024/2025.

Ulosi wa nyengo ya m’dzinja la 2025/2026 mwachidule.

Mwachidule ulosiwu uli motere:

a) Kagwedwe ka mvula.

October mpaka December 2025. Madera ambiri mdziko muno akuyembekezereka kulandira mvula yamlingo okhazikika kapena kuposera apo, ngakhale madera ena a chigawo chaku mpoto akuyembekezereka kulandira mvula ya mulingo okhadzikika kapena kuchepera apo (map A). Pali chiyembekezo choti mwezi wa November madera ambiri adzakhala ndi mvula ya mlingo okhazikika kapena kuchepera apo.

January mpaka March 2026. Tiyembekezere mvula yamlingo okhazikika kapena kuposera apo madera ambiri ngakhale madera ena am’maboma awa; Mchinji, Dowa, Kasungu ndi Lilongwe akhoza kulandila mvula ya mlingo okhadzikika kapena kuchepera apo (map B). Pali chiopsezo choti dziko lonse la Malawi mu mwezi wa February kudzakhala mvula ya mlingo okhadzikika kapena kuchepera apo.

b) Kuyamba kwa nyengo ya dzinja.

Nyengo ya dzinja ikuyembekezereka kuyamba mochedwerako ndi masabata awiri m’madera ambiri. Izi zikutanthauza kuti nyengoyi idzayamba m’masiku apakati pa mwezi wa December. Koma madera ena am’chigawo cha kumwera monga; Blantyre, Thyolo, Zomba, Mulanje ndi Chiradzulu, nyengo yadzinja ikuyembekezereka kudzayamba mu nthawi yake, pakati pa mwezi wa November. Madera ena a boma la Mchinji nyengo yadzinja ikuyembekezereka kudzayamba m’masiku apakati kapena kumathero a mwezi wa November. Pali nkhawa yoti chiyambi cha nyengo ya dzinja chikhoza kukhala chosakhazikika.

c) Mathero a nyengo ya dzinja

Madera ambiri a dziko lino ayembekezere kuti nyengo yadzinja idzatha mu nthawi yake kapena mochedwerako imene ili kumathero a mwezi wa March kufikira kumayambiliro a mwezi wa April. Koma madera ambiri a m’chigawo chapakati ndi kumpoto nyengo yadzinja ikuyembekezereka kufika kumapeto m’masiku apakati pa mwezi wa April, ngakhale madera ena ochepa nyengoyi idzatha kumapeto a mwezi wa April.

d) Kutalika kwa nyengo ya dzinja

Nyengo ya dzinja ya 2025/2026 ikuyembekezereka kukhala yamasiku pafupifupi 130 kufikira 140 m’madera ambiri. Mlingowu ndi wa m’mene umayenera kukhalira, komabe madera ena am’maboma apakati ndi kumpoto akuyembekezereka kukhala ndi nyengo yadzinja yaifupi.

e) Katenthedwe mu nyengo ya dzinja

Tiyembekezere muyeso wakatenthedwe kudzakwera kwambiri kuposa mlingo okhazikika mu nyengo ya chilimwe maka miyezi ya December ndi February koma mu mwezi wa January pali chiyembekezo choti madera ambiri am’chigawo chapakati adzakhala ndi muyeso ozizilirako kuposa mlingo okhazikika. Katenthedwe aka kadzapereka chiopsezo chakutentha moonjeza (Heatwave).

(Download full update here 👇 )