
Kuyambira mawa Lolemba pa 10 March kufika Lamulungu pa 17 March 2024, tiyembekezere nyengo ya mitambo ndi mvula ya mabingu m’madera ambiri yomwe igwe. Izi zikhale chonchi kamba ka dera lodzetsa mvula lotchedwa ITCZ lomwe lakhazikika pa Malawi. Chiopsezo chakusefukira kwa madzi chikhala chokwera m’madera ena monga m’madera am’mphepete mwa nyanja ya Malawi, komanso m’madera otsika ndi m’malo omwe kumachitika madzi osefukira pafupipafupi. Mphepo yamphamvu ya Mpoto idzayamba kuomba panyanja makamaka Lachiwiri 12 mpaka Lachisanu pa 15 March, ili ndi chenjezo kwa asodzi ndi onse ogwiritsa ntchito nyanja kuti akhale tcheru ndi osamala ndi bwino osalowa pa nyanja m’nyengo ya ulosiwu. Padakali pano dera lampweya opepuka lomwe lili m’njanya ya m’chere ya India pakati pa dziko la Madagascar ndi Mozambique litha kuchuluka nyonga ndikukhala Namondwe wotchedwa FILIPO pakati pa 11 mpaka 12 March 2024. Dera la lampweya opepukali likuyembekezeka kumayenda molungika kudziko la Mozambique kenako lizilowera kumwera kwa dzikoli ndipo litha kubwereranso m’nyanjayi India yi Lachitatu pa 13 March. Namondweyu akafika ku Mozambique akhoza ku kulimbikitsa nyengo ya mphepo yamphamvu komanso mvula m’madera ena akum’mwera kwa Malawi komwe alinso pa chiopsezo cha madzi osefukira monga ku Mulanje, Phalombe, Chiradzulu, Thyolo, Blantyre, Mwanza, Nsanje ndi Chikwawa.