
Kuyambira mawa Lolemba pa 4 March kufika Lamulungu pa 10 March 2024, tiyembekezere nyengo ya mitambo ndipo kugwa mvula ya mabingu m’madera ambiri yomwe igwe ya mphamvu m’madera ochulukirapo makamaka m’madera okwera, am’chigawo cha kumpoto komanso am’mphepete mwa nyanja ya Malawi. Izi zikhale chonchi kamba ka dera lodzetsa mvula lotchedwa ITCZ. Chiopsezo chakusefukira kwa madzi chikhala chokwera m’madera ena monga m’madera am’mphepete mwa nyanja ya Malawi, komanso m’madera otsika ndi m’malo omwe kumakonda kusefukira madzi. Pali kuthekera kwakukulu kwa Namondwe kubadwa munyanja ya m’chere ya India pakati pa dziko la Madagascar ndi Mozambique musabatayi. Pakadali pano, sizinadziwike njira imene Namondweyu angatenge akabadwa.Nthambi ya Zanyengo ndi Kusintha kwa Nyengo ipitiriza kuchita kauniuni wa Namondweyu ndikukudziwitsani momwe atayendere.