Nyengo msabata ikubwerayi 9 - 15 Sept 2024

Weekly Weather Update

Mawa lolemba pa 9 September, 2024, tiyembekezere nyengo ya mphepo, yamitambo yapatali patali komanso yotentha. Izi ndi kamba ka mpweya ofunda ochokera kumvuma.

Koma kuyambira Lachiwiri pa 10 September, mpaka lachinayi pa 12 September, 2024 kudzakhala kwa nyengo yamphepo, yamitambo, yozizila komanso yamvula yamawawa. Izi ndi chifukwa cha mphepo zozizila komanso zachinyotho chochepa zochokera kum’mwera cha kumvuma.

Mphepo za mvuma ziziomba pa Nyanja koma kuyambira lachiwiri mpaka lachinayi mphepo ya Mwera ikuyembekezereka kuomba mwamphanvu ndi liwiro loposa 50km/hr.