Nyengo msabata ikubwerayi 7- 13 Oct 2024

Weekly Weather Update

Mawa lolemba pa 7 October ndi lachiwiri pa 8 October, 2024, tiyembekezere nyengo yamitambo yapatalipatali m’madera ambiri komanso mvula igwa m’madera ena makamaka akumpoto.

Kuyambira Lachitatu pa 9 October 2024, tiyembekezere nyengo ya mphepo ndi yamitambo m’madera ambiri komanso mvula idzagwa m’madera ena.

Mphepo iziomba mwamphanvu nthawi zina pa nyanja zathu.