
Tiyembekezere nyengo ya dzuwa, ya changululu ndi yotentha kwambiri kupitirira mpaka masana a Lachiwiri pa 1 October, 2024.
Koma, kuyambira usiku wa Lachiwiri pa 1 October mpaka Lamulungu pa 6 October 2024, kudzakhala kwa mitambo, kwa mphepo ndipo madigiri akatenthedwe adzatsika, komanso kudzagwa mvula m’madera ochuluka yomwe idzagwa mwa mphamvu ndi ya mabingu m’madera ena.
Mphepo ya Mwera idzawombanso pa nyanja ya Malawi ndi nyanja zina kuyambira usiku wa Lachiwiri pa 1 October