
M’sabatayi, madera ena apitilira kulandira mvula, yomwe ikuyembekezeka kugwa makamaka m’madera am’mphepete mwa nyanja ya Malawi ndi ena am’zigawo za kumpoto komanso pakati kamba ka dera lodzetsa mvula la I.T.C.Z (Inter-Tropical Convergence Zone). Palinso kuthekera kwakukulu kwa Namondwe kubadwa m’nyanja ya m’chere ya India pakati pa mayiko a Madagascar ndi Mozambique (Mozambique Channel) pofika Loweruka lino pa 08 March, 2025.