Nyengo msabata ikubwerayi 26 Aug- 1 Sept 2024

Weekly Weather Update

Kuchokera mawa Lolemba pa 26 August 2024 mpaka lachinayi pa 29 August 2024, tiyembekezere nyengo ya mphepo, yamitambo yapatali patali komanso yotentha. Izi ndi kamba ka mpweya ofunda ochokera kumvuma. Koma pomafika madzulo a lachinayi kudzakhala kutayamba nyengo ya Chiperoni yomwe ndi yamphepo, yozizila komanso yamvula yamawawa ndi chifunga. Izi ndi chifukwa cha mphepo zozizila komanso zachinyotho zochokera kumwera cha kumvuma. Mphepo ya mvuma idziomba pa Nyanja zathu nthawi zina koma kuyambira lachinayi madzulo mphepo ya Mwera ikuyembekezereka kuomba mwamphanvu.