NYENGO M’SABATA IKUBWERAYI
Kuyambira mawa, Lolemba pa 25 November 2025, tiyembekezere nyengo ya mitambo ya patalipatali kuphatikizapo nyengo yofunda, komaso ya mvula ya mabingu yomwe izizagwa ya mphamvu m’madera ena ochepa makamaka a m’chigawo chaku m’mwera monga mapu ali Kumanjawa akuonetsera. Mvula ikhala yochepa kuyerekeza ndi sabata yatha.