Nyengo msabata ikubwerayi 23- 29 Sept 2024

Weekly Weather Update

Kuyambira mawa lolemba pa 23 September mpaka lachiwiri pa 24 September, 2024, tiyembekezere nyengo ya mphepo, yamitambo komanso yamvula yowaza m’madera ena. Izi ndi kamba ka mphweya ozizila komanso wachinyontho omwe ukuchokera kumwera chakumvuma.

Koma kuyambira lachitatu pa 25 September, mpaka lamulungu pa 29 September, 2024 kudzakhala kwa nyengo yadzuwa, changululu komanso yotentha kwambiri. Izi zichitika chifukwa cha mphepo zomwe zikhale zofunda zochokera kumvuma.

Mphepo ya Mwera ikuyembekezereka kupitilira kuomba mwamphanvu ndi liwiro loposa 50km/hr kufikira lachiwiri koma pofika Lachitatu mphepo za mvuma ziziomba pa Nyanja zathu nthawi zina.