
Kuyambira pa Lolemba pa 2 mpaka Lachitatu pa 4 September, 2024 tiyembekezere nyengo Chiperoni kupitilira, yomwe ndi nyengo yamphepo, yozizira ndi mitambo yochuluka komanso mvula yowaza ndi yamawawa komanso chifunga. Pa Nyanja ya Malawi, Chilwa ndi nyanja zina pazikhala mafunde aatali chifukwa cha mphepo yamphamvu ya Mwera yomwe idzachepe mphamvu Lachitatu madzulo. Nyengoyi ipitilira chifukwa cha mphepo zachinyontho kuchokera kum’mwera chakumvuma kufika ku Malawi.
Pali chiyembekezo choti kudzayamba kukhala nyengo yadzuwa ndi yofunda kuyambira Lachinayi mpaka kumathero kwa sabatayi, komabe nyengo yozizira pang’ono idzapitilira usiku ndi m’mawa kamba ka mphepo zofundirapo kuchokera kumvuma.