Nyengo msabata ikubwerayi 19-25 August 2024

Weekly Weather Update

Kuyambira mawa pa 19 August mpaka Lachinayi masana pa 22 August 2024, kukhala kwa mphepo ndi kwa fumbi nthawi zina ndipo tiyembekezerenso nyengo ya changululu, ya dzuwa ndi yotentha masana. Usiku ndi m’bandakucha kukhala kwa nyengo yozizira makamaka m’madera okwera komanso am’chigawo chapakati. Izi ndi kamba ka mpweya operewera chinyontho omwe ukuchokera ku mvuma m’nyanja ya m’chere ya India. Koma, mvula yowaza igwa m’madera ochepa am’chigawo cha kumpoto.

Kuyambira Lachinayi madzulo pa 22 August 2024, tiyembekezere nyengo yamphepo, yamitambo, yozizira ndi ya chifunga komanso mvula yowaza ndi yamawawa idzagwa m’madera ena ochepa makamaka am’zigawo za kum’mwera ndi kumpoto.

Mphepo yamphamvu ya Mwera ya liwiro la 45km/h ikuyembekezeka kudzachititsa mafunde owopsa otalika 1.5m panyanja ya Malawi, ya Chilwa komanso pa nyanja zina. Izi zidzakhala chonchi chifukwa cha mphepo yozizira komanso ya chinyontho yochokera kumwera chakumvuma kufalikira ku Malawi. Nyengoyi idzachepa mphamvu Lamulungu lino pa 25 August 2024.