NYENGO M’SABATA IKUBWERAYI
Kuyamba mawa lolemba pa 17 November 2025, tiyembekezere nyengo yofunda, yamitambo ndi yamphepo komanso ya mvula yamabingu yomwe madera ena idzigwa yamphamvu kuyambira kumwera kumafalikira madera akumpoto kwadziko lino. Izi ndi kamba ka nkumano wa mphepo zochokera kumwera komanso zochokera kumpoto zomwe zimatchedwa kuti ITCZ.