Nyengo msabata ikubwerayi 12-18 Jan 2026

Weekly Weather Update

NYENGO M’SABATA IKUBWERAYI

Kuyambira mawa lolemba pa 12 January kufikira lachitatu pa 14 January 2026, tiyembekezere nyengo yotentha ndi yamitambo yapatali patali komanso mvula ya mabingu ya apo ndi apo kamba ka mphepo zochokera kumpoto chakunvuma. Mvula idzakhala ikufalikira m’madera ambiri pofika lachinayi pa 15 January 2026 pomwe mphepozi zikuyembekezereka kukumana ndi mphepo zochokera kumpoto cha kuzambwe.