Nyengo msabata ikubwerayi 12-18 August 2024

Weekly Weather Update

NYENGO M’SABATA IKUBWERAYI

Kuyambira Lolemba pa 12 August mpaka Lachitatu pa 14 August nyengo yadzuwa, yotentha, yafumbi ndi changululu ipitilira m’madera ambiri. Usiku ndi m’bandakucha kuzikhala kwa nyengo yozizira mmadera ena.

Kenako kuyambira Lachinayi pa 15 August tiyembekezere nyengo yamphepo ndi mitambo yochuluka ndi kuthekera kwa mvula yowaza ndi yamawawa mmadera ena kuyambira m’madera akum’mwera kufalikira pakati ndi kumpoto. Panyanja zathu monga ya Malawi ndi Chilwa padzakhala mafunde okula chifukwa cha mphepo ya Mwera m’nthawiyi.

Izi zizakhala chonchi kamba ka mphepo zozizira komanso zachinyontho kuchokera m’nyanja yamchere ya India kufikira ku Malawi.