NYENGO M’SABATA IKUBWERAYI
Kuyamba mawa lolemba pa 1 December 2025, tiyembekezere nyengo yofunda, yamitambo ndi yamphepo m’madera ambiri komanso ya mvula yamabingu yomwe nthawi zina idzigwa yamphamvu maka m’madera akumwera. Izi ndi kamba ka nkumano wa mphepo zochokera kumwera chakumvuma komanso zochokera kumvuma.