DCCMS ifikira achinyamata ku Machinga

Wolemba: Alick Chibanthowa

29 Mar, 2025 News

Ngati mbali imodzi yokonzekera mwambo wapa chaka wokumbukira zanyengo pa dziko lonse, omwe udzachitike Lachisanu pa 11 April pa bwalo la mpira la Machinga TTC, kuyambira 08:30 m’mawa, Nthambi Yowona Zanyengo ndi Kusintha kwa Nyengo (DCCMS), inafikira achinyamata m’ma sukulu osiyanasiyana ku Machinga pa 25 ndi pa 26 March, 2025. Cholinga chake, chinali kumema achinyamata a m’bomali kudzatenga nawo mbali pa mwambowu komanso kuwaphunzitsa zambiri zokhudza kusintha kwa nyengo.

Joster Muhalu

Joster Muhalu kufotokoza za kusintha kwa nyengo.

Amad Yusufu, m’modzi mwa ophunzira a pa sukulu yoyendera ya Matanda, anati anali osangalala kwambiri ndi maphunzirowa ndipo anatsindika kufunika kwa maphunziro okhudza zanyengo komanso kusintha kwa nyengo kwa achinyamata.

Maphunzirowa anakonzedwa ndi chithandizo chochokera ku bungwe la CEPA komanso ku Banki Yaikulu ya padziko lonse kudzera m’mapolojekiti a MWASIP komanso CREWS.

Ngakhale kuti mwambowu umachitika pa 23 March chaka chilichonse, chaka chino wasinthidwa chifukwa cha Namondwe Jude, yemwe anakhudza madera ambiri am’zigawo zakumwera m’mwezi wa March.

Mutu wa chaka chino ndi “umodzi pothana ndi zotsamwitsa za machenjezo a ngozi zokhudzana ndi nyengo”, omwe ukutsindika kufunika kwa mugwirizano wa padziko lonse omwe ungachititse kuti aliyense, kulikonse, akhale ndi mwayi olandira ma chenjezo a zanyengo munthawi yake. Izi zikugwirizananso ndi loto la bungwe la United Nations lakuti pofika chaka cha 2027 aliyense, kulikonse azitha kulandira machenjezo amsanga.

WhatsApp Image 2025-03-25 at 11.36.14

Achinyamata kulimbikitsidwa

Pamwambowu achinyamata osiyanasiyana adzafotokoza momwe kusintha kwa nyengo kwa khudzira madera awo kudzera mu nyimbo, zisudzo komanso ndakatulo. Mulendo olemekezeka pa mwambowu adzakhala Nduna Yazachilengedwe ndi Kusintha kwa Nyengo, a Dr. Owen Chomanika.