Chidwi Cha A Malawi pa Mauthenga a Zanyengo Chikukula M’masamba a Mchezo

By Alick Chibanthowa

22 Jul, 2025 Article

Anthu ambiri akuchita chidwi ndi mauthenga a zanyengo pa masamba a mchezo. Izi zikuonekera pa kuchuluka kwa a Malawi omwe akutsatira mauthenga a zanyengo kudzera pa WhatsApp ndi pa Facebook, komanso masamba ena. Mwachitsanzo, tsamba la pa Facebook, la Nthambi Yowona Zanyengo ndi Kusintha kwa Nyengo lotchedwa Department of Climate Change and Meteorological Services tsopano liri ndi olitsatira opitirira zikwi makumi asanu ( 50, 000). Pomwe tsamba la pa WhatsApp la Nthambiyi, liri ndi olitsatira opitirira zikwi khumi ndi zisanu ( 15,000).

Nkhaniyi yadzetsa chisangalalo pakati pa a namandwa a zanyengo aku Nthambiyi. Chisangalalochi chabwera kamba kozindikira kuti anthu ambiri tsopano azilandira mauthenga a zanyengo monga okhudza a namondwe , mphepo ya Mwera komanso mvula, munthawi yake.

Nthambi Yowona Zanyengo ndi Kusintha kwa Nyengo imagwiritsa ntchito masamba amchezo monga WhatsApp, Facebook, X , YouTube ndi ena otero ngati njira imodzi yofalitsira mauthenga a zanyengo. Nthambiyi imachita izi ndi choringa chothandidza kupulumutsa miyoyo, kutukula chuma cha dziko komanso kupulumutsa katundu.