Nyengo msabata ikubwerayi 28 Oct - 3 Nov 2024

Weekly Weather Update

Tiyembekezere nyengo ya mvula ya mabingu ndi mphepo ya mkuntho mmadera ena. Nyengoyi idzayamba Lolemba m’madera am’zigawo za pakati ndi kumpoto ndipo idzafalikira m’madera am’chigawo cha kum’mwera pofika Lachiwiri pa 29 October 2024. Izi zikhala chonchi kamba ka dera lodzetsa mvula lomwe likuyembekezeka kukhudza nyengo ya kwathu kuno m’sabatayi. Nyengo yotentha monyanyira ndi modetsa nkhawa idzachepa mphamvu pofika Lachitatu pa 30 October 2024